PEMPHERO LA MTENDERE (#13480)

O Inu Ambuye wokoma mtima! Inu mwalenga mtundu wonse wa anthu kuchokera kwa kholo limodzi. Inu mwalamulira kuti onse adzakhala abanja limodzi. Pamaso panu poyera iwo ali antchito Anu, ndipo mtundu wonse wa anthu wafungatiridwa pansi pa Chihema Chanu; onse asonkhana pamodzi ku Gome la Kuolowamanja Kwanu; onse awalitsidwa kupyolera mu kuwala kwa chisamaliro Chanu.  
O Mulungu! Inu Ndinu wokoma mtima kwa onse, Inu mwapereka kwa onse zosowa zawo, mumafungatira onse, mumapatsa moyo kwa onse. Inu mwawapatsa yense waiwo ndi iwo onse luso la nzeru, ndipo onse amizidwa mu Nyanja ya Chifundo Chanu.  
O Inu Ambuye wokoma mtima! Gwirizanitsani onse. Pangani kuti zipembedzo zigwirizane ndipo pangani kuti mitundu yonse ikhale mtundu umodzi, kuti aonane wina ndi mzake ngati abanja limodzi ndipo dziko lonse lapansi ngati kukhomo kwawo kumodzi. Azikhalira pamodzi mu kumvana kwangwiro.  
O Mulungu! Kwezani m’mwamba kwambiri mbendera ya umodzi wa mtundu wa anthu. O Mulungu! Khazikitsani Mtendere Waukulu Koposa. Umbani Inu, O Mulungu, mitima yonse pamodzi. O Inu Atate wokoma mtima, Mulungu! Sangalatsani mitima yathu kupyolera mu pfungo labwino la chikondi Chanu.  
Walitsani maso athu kupyolera mu kuwala kwa Chitsogozo Chanu. Sangalatsani makutu athu ndi kukoma kwa Liu Lanu, ndipo tifungatireni mu Tchinga la Chisamaliro Chanu. Inu Ndinu Wanyonga ndi Wamphamvu, Inu ndi Wokhululukira ndipo Ndinu Nokha Amene simulabadira zoperewera za mtundu wonse wa anthu.

-`Abdu'l-Bahá
-----------------------

